A Polisi amanga mzimayi, abambo awiri kamba kopezeka ndi chamba
A Polisi kwa Jenda m’boma la Mzimba amanga mayi wina ndi amuna awiri chifukwa chopezeka ndi fodya wa Chamba pamalo otchedwa Luviri m’bomali pomwe amadikira galimoto kuti apite ndi katunduyu ku Lilongwe.
Malinga ndi ofalitsa nkhani za polisi ya Jenda a Macfarlen Mseteka, atatuwa ndi a Pililani Phiri a zaka 46, a Stanley Mologeni a zaka 34 ndi a Ryford Magiwa a zaka 37.
A Mseteka ati atatuwa anawapeza ndi mabeseni khumi a fodyayu okungidwa ngati anyamula tomato olemela makilogalamu 11 lirilonse ndi thumba limodzi lolemela makilogalamu 10.
Iwo ati atatuwa awamanga dzulo madzulo pomwe munthu wina yemwe anali limodzi anakwanitsa kuthawa.
A Pilirani Phiri amachokera m’boma la Phalombe, a Stanely Mologeni amachokera m’boma la Dedza pomwe a Ryford Wagiwa amachokera m’boma la Thyolo koma onsewa amachita malonda awo ku Lilongwe.
Follow and Subscribe Nyasa TV :