Sizinafike poipa zinthu, zikadzafika ndizaimba nyimbo – watelo Lucius Banda

Advertisement

Mkulu uja anaimba nyimbo zodzudzula misonkho yochuluka, anaimbanso zodzudzula tsankho, ndi kudzudzulanso kukonda ma ulendo kwa adindo, lero ati zinthu ku Malawi kuno sizinafike poipa pofuna kudzudzula.

Lucius Banda amene ndi mlangizi wa President Lazarus Chakwera anauza anthu pa msonkhano wina wandale kuti asiye kukokomeza mavuto a ku Malawi kuno.

“Zinthu zikavuta mumaonela a nsembe ndi ena a mpingo kudzudzula. Komanso Lucius Banda amaimba nyimbo,” iye anatelo kenako kutsimikiza kuti sanapange zonsezo, kusonyeza zinthu ziliko bwino.

Malinga ndi Banda, zinthu zakwela mtengo pa dziko lonse lapansi ndipo kuimba mlandu a Chakwera ndi boma lawo la Tonse ndi kulakwa basi.

“Ndinali ku South Africa ma sabata awili apitawo, kumenekonso zinthu zakwela,” anatelo.

Iye anaonjezelaponso kuti zinthu zinaonongeka mu zaka 6 ndipo palibe chifukwa choyembekezela kuti zingakonzedwe mu chaka chimodzi.

“Kunali chifwilimbwiti zaka 6 zapitazi, sizingatheke kuzikonza mu chaka chimodzi,” anaonjezelapo Banda.

Iye anatinso mavuto amene a Malawi akukumana nawo adza kamba ka mliri wa Kovidi.

 

Advertisement

3 Comments

  1. Sitingadandaule ngakhale mutati musayimbe nyimboyo. Vuto taliona kuti inunso munali so ndikafika ndi Boma linapita lija. Munthu wanzeru ngati I uyu simungayankhule choncho. Izi zikungotiuza ife kuti inuyo ABanda nanunso muli ndi vuto LA Utsogoleri. Zindikira kuti Oyimba sinunokha paMalawipa.

  2. A chisilu awa ayambano kuyamikila zolakwika chifukwa wapasidwa mpando ukadwala usamalire kupempha chithandizo uzimupempha chakwela wakoyo ndi wankulu mutu wakoyo chilima

Comments are closed.